"CHIGAWO CHACHIWIRI ASEWERA NDI MA DOTOLO" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wadandaula kuti mchigawo chachiwiri cha masewero awo, mpira unayima kwambiri pomwe madotolo amangokhalira kulowa mu bwalo kuti athandize osewera a Kamuzu Barracks.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 ndi timu ya KB pa bwalo la Nankhaka lachinayi masana ndipo wayamikira anzawowa kamba kokwanitsa kuwagonjetsa.
"Anali masewero abwino kwambiri tinayamba bwino koma timadziwa kuti anzathuwa abwera molimba kwa Ife chifukwa tawagonjetsako kawiri motsogozana nde tiwayamikire kuti achita bwino." Anatero Nyambose.
Iye anati timuyi inakwanitsa kusewera mu chigawo choyamba ndi anzawowa pomwe mchigawo chachiwiri kunachuluka kumenyera mpira panja komanso kugwaigwa.
Timuyi yataya mwayi wotuluka ku chigwa cha matimu omwe akhonza kutuluka mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 17 pa masewero 20 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores