"OSEWERA ENA SAKUDZIWA CHOMWE ANABWERERA" - YASIN
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Rodgers Yasin, wati ntchito imene alinayo ndi yokonza kaganizidwe ka osewera kuti ayambe kuganiza za mpira poti ena akumachulutsa zibwana mmasewero awo.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Premier Bet Dedza Dynamos ndipo wati osewera ena akumachita zinthu ngati sakudziwa ntchito yawo zomwe akufunika kuti azikonze.
"Sikuti chilipo chasintha, sitinapume kwenikweni mukudziwa sabata yatha tasewera ndi Bullets nde apa tikubwereranso. Chimene tikulimbana nacho ndi kaganizidwe ka osewera chifukwa ena akuoneka kuti sakudziwa chomwe anabwerera ndi ntchito yawo nde tikuyenera kukonza zimenezo." Anatero Yasin.
Iye wati kusamuka kwa timuyi kupita ku Balaka zikakhala zabwino chifukwa akasewera pa anthu oti sakuwadziwa nde zoyankhula zimachepa.
Bangwe ili pa nambala 15 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi asanu ndi anayi (9) pa masewero 15 mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores