"NDI NTHAWI YOTI SILVER IMVE ZOWAWA" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wati timu yake ikuyenera kugwiritsa ntchito mwayi wosewera pakhomo kuti apeze chipambano pomwe Silver Strikers inawamenyako ku Lilongwe.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi Mabanker loweruka pa bwalo la Karonga ndipo wati chimene akufuna iwo ndi chipambano kuti apitilire kuyenda bwino mu ligi.
"Sikuti tikungofuna kubwenzera kokha komanso kugwiritsa ntchito mwayi wosewera pakhomo chifukwa kwawo anatichinya nde tiyesetsa kuti Iwo amve zowawa lowerukali." Anatero Kaunda.
Iye watinso osewera mmodzi, Alfred Chizinga, wabwerera kuchokera kovulala ndipo ena omwe alengeza kuti awatenga sapezeka pa masewerowa chifukwa choti akukonzabe za mapepala awo.
Timuyi ili pa nambala yachikhumi ndi chimodzi mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 19 pa masewero omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores