"BAKA NDI TIMU YOTI SITINAYIMENYEKO" - KAMWENDO
Mphunzitsi wogwirizira watimu ya Creck Sporting Club, Joseph Kamwendo, wati timu yake siyipita mophweka ikamakumana ndi Baka City poti yakanika kupeza chipambano pa masewero awiri omwe akumana.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo omwe aseweredwe pa bwalo la Dimba loweruka ndipo wati akufunitsitsa atayambira pomwe anasiyira mu chigawo choyamba.
"Tinamaliza ndi Chipambano 2-0 ndi Dedza Dynamos nde tikufunitsitsa titakayambira pomwe paja kuti mchigawo chachiwirichi tichite bwino. Sitipita mophweka chifukwa tinafanana mphamvu kwawo ndipo inatitulutsa mu FDH Bank nde tikayesetsa kumenyera nkhondo kuti tichite bwino." Anatero Kamwendo.
Iye wati anyamata awiri aku Nigeria komanso Chris Lwemba atha kuoneka pa masewero awowa poti akhala nawo kwa nthawi tsopano.
Creck ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ili ndi mapointsi 23 pa masewero 15 omwe yasewera mu ligi ya TNM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores