MWASE SANAKWANILITSE ZOMWE ANAPATSIDWA
Mphunzitsi wogwirizira watimu ya Mighty Mukuru Wanderers ali pawiri poti akhonza kumupatsiratu ntchitoyi kapena kukhalabe wachiwiri wa mphunzitsi yemwe timuyi itha kulemba poti wakanika kukwanilitsa zomwe anauzidwa kuti achite.
Malingana ndi nyuzipepala ya Nation, wina mu timu ya Wanderers anawauza kuti Mwase anapatsidwa kuti amalize pa nambala yoyamba chigawo choyamba chikamatha komanso kuti afike mu ndime yotsiriza ya chikho cha FDH Bank.
Timuyi ili pa nambala yachiwiri mu ligi pomwe akusiyana mapointsi asanu ndi anayi (9) ndi Silver Strikers komanso anatuluka kale mu chikho cha FDH Bank atagonja 1-2 ndi FCB Nyasa Big Bullets.
Ndipo yemwe amayang'anira za aphunzitsi akutimuyi, Tiyasomba Banda, wati akuluakulu akuunikirabe mmene Mwase wachitira koma chiganizo pa mpandowu chidziwika posachedwa.
Mwase anatenga mpandowu kutsatira kutula pansi kwa mphunzitsi wamkulu, Nsanzurwimo Ramadan.
Source: Nation 📷: Noma media
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores