BULLETS YALEMBERA FAM PA KAMWENDO
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yalemba kalata yopita ku bungwe la Football Association of Malawi kudandaulapo pa mmene yalepheretsedwa kugula osewera wa Premier Bet Dedza Dynamos, Promise Kamwendo, ngakhale kuti anali atalipira kale zonse.
Izi zadza kutsatira kuti katswiriyu anapita kukasaina mgwirizano ndi Mighty Mukuru Wanderers ngakhale kuti anali atamvana ndi FCB Nyasa Big Bullets poyamba ndipo pobwera ku Blantyre amadzasaina mgwirizano ndi Bullets.
Mapalestina alembera timu ya Dedza kuti ifotokoze mmene zayendera kuti osewerayu tsopano apite ku Wanderers koma iwo atagwira kale K3 million ya osewerayu ndipo alemberanso mkulu woona za kusintha matimu kwa osewera, Cassper Jangale, yemwe watsimikiza kuti kalata walandira.
Koma polemba pa tsamba lake la mchezo, mmodzi mwa atolankhani okhalitsa, Steve Liwewe Banda, wati zomwe zachitikazi ndi zofanana ndi Moises Caicedo mmene matimu a Liverpool komanso Chelsea ankamufuna komabe FCB Nyasa Big Bullets i
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores