"ATIONETSE KAYE UMBONI OTI ANAGULITSANA" - JANGALE
Mkulu woyendetsa za kusintha matimu kwa osewera ku bungwe la Football Association of Malawi, Cassper Jangale, anauza timu ya FCB Nyasa Big Bullets kuti singayime ndi dongosolo lomalizitsa kusintha timu ya Promise Kamwendo kuchoka ku Premier Bet Dedza Dynamos kupita ku Mighty Mukuru Wanderers pokhapokha alembe dandaulo moyenera.
Mkuluyu anayankha izi kutsatira uthenga womwe timuyi inalembera FAM kuti achedwetse kaye kumalizitsa za kusintha timu pa katswiriyu kamba koti zipanayende bwino.
Koma Jangale wati izi sizingatero pokhapokha abweretse umboni kuti anagulitsanadi osewerayu nde pamenepo apeza poyambira pa nkhaniyi.
"Bullets inatilembera uthenga kudzera pa Email kutiuza kuti tisapitilize kumalizitsa zonse za Promise Kamwendo koma tawauza kuti alembe dandaulo labwinobwino ndi zifukwa zomwe tiyimire. Ationetse kuti anagulitsanadi nanga panali pempho loti akufuna osewerayu komanso linavomeredwa kenako tiyambapo." Anatero Jangale poy
Palibe umboni Wina uliwonse oti bullets inagula kamwendo . Ndalama zomwe anapereka inali yoti apangire transport iye ndi manager wake from Dedza to Blantyre . Osati ndi signing fee AI .
Ngati player asintha maganizo Ake Ali mu njira palibe chifukwa chopitira kukadandaula ku FAM AI . Iwo abullets akanakhala ena akangolembera Kalata a Dedza Dynamos Kuti abwezeredwe ndalama zawo finish.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores