"OSEWERA AMBIRI AMU LIGI ANADUTSA ZAKA 30" - TWAHA
Mmodzi mwa akatswiri oyankhulapo komanso kulemba nkhani za masewero, Twaha Chimuka, wati Osewera ambiri amdziko muno amaoneka ngati ali ndi zaka zochepa poti amadziwika mochedwa koma ambiri ndi akuluakulu.
Iye amayankhulapo potsatira kubwenzedwa kwa katswiri wa Mighty Mukuru Wanderers, Lawrence Chaziya, kuchokera ku timu ya TP Mazembe kamba koti zichitochito zake sizimagwirizana ndi zaka zomwe analemba
Iye anapereka Chitsanzo pa masewero a Soshozi omwe osewera akuluakulu amasewera kuti amaonekeratu kuti mphamvu zawo ndi zamasewero amenewo chifukwa cha zaka ndipo munthu ukukula zambiri sizimatheka.
"Nkhani ya zakayi ndi yeniyeni ndithu ku Malawi kuno kaya osewera timakhala kuti tamudziwa mochedwa nde osewera wa zaka 20 amakhala wa zaka 15 koma kunena chilungamo, osewera ambiri mu ligi yathu anadutsa zaka 30," anafotokoza Chimuka.
Iye koma wapempha timu ya Mighty Mukuru Wanderers kupeza katswiri oyang'ana za kaganizidwe ka munthu k
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores