NKHANI
Katswiri wa Mighty Mukuru Wanderers, Christopher Kumwembe, tsopano akulowera ku Zambia mu tsiku la lero kutsatira kuti zonse zatheka zoti apite kutimu ya Green Buffaloes yomwe imasewera mu ligi yaikulu mdzikomu.
Kumwembe wakhala akufunidwa ndi timuyi koma Wanderers imamukaniza ndipo Wanderers imanukanizanso kupita ku Power Dynamos komwe timuyi inapempha kuti akayeze mwayi kwa masiku angapo.
Koma Kumwembe tsopano akupita ku Zambia pomwe matimu a Buffaloes ndi Wanderers amvana chilichonse ndipo katswiriyu akasewera mu MTN Super League ku Zambia.
Wanderers inakakamiza kusaina Promise Kamwendo kuchokera ku Premier Bet Dedza Dynamos poti amasaka mlowammalo wake kutimuyi.
📷: MH Photography
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores