"ANYAMATA AKUPHONYA KWAMBIRI" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civo United, Abbas Makawa, wati kuchoka kwa Binwell Katinji kutimuyi kwapangitsa kuti asapeze anyamata odalilika ogoletsa zigoli ndi chifukwa chake akuphonya kwambiri mipata yochuluka.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 1-0 ndi timu ya FOMO pa bwalo la Civo ndipo wati anali masewero ovuta koma zilibwino poti apambana atagonja masewero atatu.
"Anali masewero ovuta kwambiri, timadziwa kuti avuta chifukwa anyamata ali ndi phuma kamba kophonya mipata komabe ndine okondwa poti tapambana. Mwina panopa tilibe katswiri wokhazikika oti azimwetsa zigoli, anachoka Binwell Katinji sitinapeze mlowammalo nde tiphunzitsabe omwe tili nawowa afikaponso." Anatero Makawa.
Timu ya Civo tsopano yafika pa nambala yachikhumi ndi chimodzi (11) pomwe yapambana kawiri ndi kugonja katatu ndipo ili ndi mapointsi asanu ndi imodzi (6).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores