"ANATISOKONEZA NDI MMENE ANASINTHIRA A BULLETS" - MWASE
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Meke Mwase, wati kusintha kumene timu ya FCB Nyasa Big Bullets inachita mchigawo chachiwiri kunawasokoneza mpake anakanika kuteteza chigoli chawo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 1-1 ndi timuyi pa bwalo la Kamuzu ndipo wati mphamvu za Bullets zinachuluka mchigawo chachiwiri mpake anapezesa chigoli.
"Tasewera bwino kwambiri mu CHIGAWO choyamba koma tikanakhalanso kuti ifeyo timatsalira tikanatha kubweranso mwa mphamvu nde kusintha komwe anapanga anzathu kunatisokoneza, analowetsa anyamata ataliatali omwe anasokoneza kumbuyo kwathu." Anatero Mwase.
Iye wati vuto lomwe akukumana nalo ndi lophonya mipata yochuluka ndipo wati ndi mbali yomwe timuyi ikukonza kuti iyende bwino.
Timu ya Wanderers ikadalibe pa nambala yachitatu pomwe ili ndi mapointsi 9 pa masewero asanu pomwe yapambana kawiri ndi kufanana mphamvu katatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores