"AKHALA MASEWERO OVUTA KWAMBIRI" - MWANSA
Mphunzitsi watimuyi ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati akuyembekezera kuti masewero atimuyi ndi Mzuzu City Hammers akhala ovuta poti anyamatawa akudziwana komanso amaonana kwambiri.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe achitike pa bwalo la Mzuzu loweruka ndipo wati ngakhale masewerowa atavute, Iwo akungopitirako kuti akachite bwino mmasewerowa.
"Tikudziwa akhala masewero ovuta kwambiri kutengera kuti matimuwa akudziwana komanso amaonerana zokonzekera poti amapangira malo amodzi koma ngakhale atavuta bwanji Ife tikupitilirako chipambano." Anatero Mwansa.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ili ndi mapointsi asanu ndi awiri (7) pomwe yafanana mphamvu kamodzi, kupambana kawiri ndi kugonja kamodzi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores