"TIKUFUNA TINYAMULE UKULU WA MZINDA WA BLANTYRE" - SAMBANI
Mtsogoleri wa osewera kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Precious Sambani, wati masewero awo ndi Mighty Mukuru Wanderers akhale ovuta poti amalimbirana ukulu wa mzinda wa Blantyre koma wati akufuna atautenga.
Iye amayankhula lachisanu patsogolo pa masewerowa loweruka ndipo wati timu yake yakonzeka kuti apeze chipambano pamwamba pa Manoma mu ligi poti akhalitsa osayigonja mu ligi.
"Takonzekera bwino masewerowa amenewa mukudziwa ndi oti timalimbana nde akhale masewero ovuta koma tilibe phuma lililonse ndipo takonzekera mmene timakonzekerera masewero aliwonse ndipo tikuyembembekezera kuchita bwino." Anatero Sambani.
Iye anati tsopano akufunitsitsa atapambana masewerowa mu ligi poti patenga nthawi chiwagonjetsereni mu 2022 ndipo wati atenga ukulu wa mzinda wa Blantyre.
Matimuwa akukumana onse ali ndi mapointsi asanu ndi atatu pomwe akwanitsa kupambana kawiri ndi kufanana mphamvunso kawiri pa masewero anayi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores