"TIKUYEMBEKEZERA MASEWERO OVUTA" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wati akuyembekezera masewero ovuta pomwe akukumana ndi Bangwe All Stars kamba koti ikuchokera koyimitsa timu yaikulu ngati Mighty Mukuru Wanderers sabata yatha.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aseweredwe lamulungu ku Aubrey Dimba Stadium ku Mchinji ndipo wati akasewerera pa bwalo lomwe iwo ankafuna kale kuti azisewererapo.
"Takonzeka bwino kwambiri ndipo anyamata onse akudziwa kufunikira Kwa masewerowa kungoti akhale masewero ovuta kutengera kuti anzathuwa anayimitsa timu yaikulu nde tidzalimbana nawo koma ifeyo tikuyang'ana chipambano pa masewerowa." Anatero Kamanga.
Iye wamema anthu ozungulira mu bomali kuti akhamukire ku bwaloli ndipo mphoto yomwe adzawapatse patsikuli ndi chipambano.
Timuyi ili pa nambala yachisanu mu ligi pomwe yapezako mapointsi asanu ndi atatu (8) kamba koti apambana kawiri ndi kufanana mphamvunso kawiri mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores