"TAPHONYA KWAMBIRI LERO" - NATHANIEL
Wachiwiri kwa othandizira kwa mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Gift Nathaniel, wati timu yawo yakanika kupeza chipambano pa masewero awo kamba koti osewera awo aphonya mipata yochuluka kwambiri.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 ndi timu ya Mighty Waka Waka Tigers pa bwalo la Karonga ndipo wati iyi yangokhala nyengo yovuta yomwe timuyi ikudutsa koma osewera abwino ali nawo.
"Tagonja ngati timu koma tinasewera bwino kungoti tayiluza kumapeto kwa masewerowa koma tinapeza mipata yambiri taphonya mwina mchigawo choyamba chija bwenzi ili 2-0 koma tinenedi kuti taphonya kwambiri." Anatero Nathaniel.
Iye wati masapota atimuyi alimbe mtima ndipo akhale nawobe osewerawa kuti chilichonse chikhale bwino kutimuyi poti ndi yabwinobwino koma mwina yangokumana ndi nyengo yoyipa.
Timuyi yangopambana masewero amodzi okha pa masewero asanu pomwe anayi anagonja ndipo ali pa nambala 13 ndi mapointsi atatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores