Juvinala: Sindimayembekezera zopita ku Bullets
Katswiri watsopano kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Andrew Juvinala, wati Bullets yakhala timu yake yakumaloto chifukwa chake sanaganizenso kangako timuyi itamufuna.
Iye amayankhula atatha kusaina mgwirizano wa zaka zitatu ndi timuyi kuchokera ku Blue Eagles ndipo wati sanaganizeko kuti timuyi itha kumufuna.
Iye wati: "Mulungu wanditsegulira njira yatsopano nde ndiyesetsa kuti ndigwire ntchito yomwe akuluakulu amdifunira kunoko nde ndine wosangalala kwambiri."
Iye wakhala wosewera wachitatu kupita kutimuyi patsogolo pa ligi ya 2025 pomwe timuyi inasaina kale Chikumbutso Henderson ndi Blessings Josephy.