Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"NDINE WOKONDWA POTI TAPAMBANA" - CHIRAMBO
Mphunzitsi watimu ya Mzuzu City Hammers, Elias Chirambo, wati ndi wokondwa kamba kopambana masewerowa awo koyenda ponena kuti anakumana ndi timu yabwino kwambiri.
Iye amayankhula atagonjetsa Creck Sporting Club 1-2 pa bwalo la Civo kuti atenge mapointsi atatu ndipo wati ndi wokondwa kamba Ka chipambanochi.
"Anali masewero ovuta kwambiri poti Creck ndi timu yabwino kwambiri nde masewero anavuta koma anyamata analimbikira ndipo ndine wokondwa poti timu yanga ndi imene yapambana ndipo kupeza chipambano koyenda sizophweka, tichisunga ndipo tikubwera nacho kwathu." Anatero Chirambo.
Timuyi tsopano ili pa nambala yachiwiri mu ligi ya TNM pomwe yakwanitsa kupambana katatu ndi kugonja kamodzi kuti akhale ndi mapointsi asanu ndi anayi (9) pa masewero anayi.
RASHID OUT FOR THREE WEEKS
Mzuzu City Hammers has announced that their captain, Yasin Rashid, will miss the team's action for three weeks or less due to injury.
Rashid was stretched off in the first half of the match that the team lost 1-0 to Mighty Waka Waka Tigers at the Kamuzu Stadium last Sunday and the team has released the extent of the injury.
According to Physiotherapist Lindie Anthony, Yasin Suffered an ankle sprain grade and said he can be back even before 3 weeks.
"Initially he was supposed to be out for 3 weeks but after receiving treatment and close monitoring there has been great improvement which can make him to be 100% fit in due course but we will not rush until he finishes the rehabilitation process," said Anthony.
The player was an important player in the team's first two games which they won against Civo United and Karonga United and managed to score a goal plus one player of the match award.
"ITS WAS NOT OUR DAY" - CHIRAMBO
Mzuzu City Hammers coach, Ellias Chirambo, conceded a defeat at the Kamuzu Stadium saying the team struggled on the midfield because of the injury of their captain Yasin Rashid.
Chirambo said this after their 1-0 defeat and said the team missed too many chances into the game that cost them to lose in the match.
"It was a good game which i think we missed a lot of chances and we were not good on the midfield after we lost Yasin [Rashid] to injury. It was not our day." Said Chirambo.
The coach further said the team will bounce back soon as he will rectify the problems encountered in the match.
Hammers remain fourth on the table as they have 6 points from their two wins and one loss in their opening three match of the league.
MZUZU CITY HAMMERS ILI PAMWAMBA PA LIGI
Timu ya Mzuzu City Hammers ikupitilira kuchita bwino pomwe yapambana masewero awo achiwiri mu ligi pogonjetsa Baka City 2-1 pa bwalo la Mzuzu.
Isaac Msiska komanso Yasin Rashid anamwetsa zigoli zatimuyi pomwe Joseph Mwambungu anapeza chopukutira misonzi zomwe zinakondweretsa mphunzitsi wamkulu, Elias Chirambo.
"Ndine wokondwa kwambiri kamba koti tapambana, sabata yatha tinavutika popita kutsogolo nde tinakonza mavuto athu, tasewera bwino ndipo tapambana. Sine wokhutira ndi mipata yomwe taphonya poti tinakonza kwambiri kutsogolo nde tikakonzanso." Anatero Chirambo.
Hammers tsopano ili pamwamba pa ligi ndi mapointsi asanu ndi imodzi (6) omwe awapeza pa masewero awiri omwe yasewera.
HAMMERS YAWINA K90 MILLION KU BETIKA
Kampani yopanga za mlosera ya Betika yasainirana mgwirizano wa zaka zitatu ndi timu ya Mzuzu City Hammers omwe timuyi izilandira K30 million pa chaka chilichonse.
Mgwirizanowu wasainidwa lachisanu ku Mzuzu komwe mwa zina amaulula zamumgwirizano wawo komanso kuonetsa unifolomu yomwe agwiritse ntchito chaka chino.
Wapampando watimuyi, Gift Mkandawire wati ndi wokondwa kamba Ka thandizoli pomwe lithandize kuti timuyi iyende bwino mu zaka zitatu zikudzazi.
"Matimu ang'onoang'ono ngati ifeyo timakumana ndi mavuto osiyanasiyana nde anzathuwa abwera nthawi yabwino atithandizako kuchepetsa mavuto omwe timakumana nawo." Anatero Mkandawire.
Ndipo mkulu wa kampani ya Betika, Gift Govati, wati akufunitsitsa atatukula luso la mchigawo chakumpoto poti kwa nthawi yaitali limavutika kuti lionedwe ndi anthu.
Timuyi iyamba kugwiritsa ntchito makaka olembedwa Betika loweruka pomwe akukumana ndi Baka City pa bwalo la Mzuzu mu masewero awo achiwiri amu 2024 TNM Su
"WE WERE OUTPLAYED DESPITE WINNING" - CHIRAMBO
Mzuzu City Hammers head coach, Elias Chirambo, said his team did not perform well and requires to improve in their next games despite securing a win against Civo United.
He said this after the match which they won 1-0 at the Mzuzu Stadium but said his team were below par because they have new boys who are learning the heat of the Elite League.
"It's good that we have won but we struggled in the game a lot, we were second on the ball there was a poor transition from the back going upfront so we need to improve so that we continue winning." Said Chirambo.
The win took Hammers up to 6th in the first week of the League with three points from one game played.
RASHID TO CAPTAIN HAMMERS IN 2024
Mzuzu City Hammers has announced the appointment of defender, Yasin Rashid, as the captain of the team in the 2024 season.
The team also has recommended Wongani Lungu and Aubrey Simbi to be his deputies in the position.
Rashid takes the role after captain, Blessings Singini left it void following his move to Mighty Mukuru Wanderers three months ago.
EKWENDENI IKUSINTHA DZINA
Timu yomwe imasewera mu ligi ya TNM, Ekwendeni Hammers yalembera kalata bungwe la Football Association of Malawi kupempha kuti isinthe dzina lake.
Timuyi yapanga chiganizo kuti tsopano izitchedwa Mzuzu City Hammers kamba koti omwe amathandiza timuyi amakhala mu mzinda wa Mzuzu chiyambireni kuyithandiza timuyi.
Mlembi watimuyi, Benjamin Thole ndiyemwe watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati padakali pano adikira chilolezo kuchokera ku FAM kuti dzinali lisinthe. Timuyi inalowa mu Supa ligi mu 2019 ndipo ikhala yachiwiri kusintha dzina chaka chino pomwe Kawinga FC inakhala Creck Sporting Club.
NIGERIAN FORWARD LEAVES EKWENDENI TO JOIN ZESCO
Ekwendeni Hammers forward, Samuel Adebiyi Adeyemi, has left the club to join the MTN Super League Zambian side, Zesco United on a 6-months deal on Thursday.
The 28 year old star has been playing for Hammers since 2021 and went to Kabwe Warriors for trials last month where he was not successful before joining Zesco.
He makes a return to Zambia after leaving Prison Leopards in 2021 to join Hammers and has played for Club Athletico in the Nigerian lower leagues.
"CHIGOLI ANAWANGOWAPATSA A BULLETS CHINATIBALALITSA" - CHIRAMBO
Mphunzitsi watimu ya Ekwendeni Hammers, Elias Chirambo, wati chigoli chomwe FCB Nyasa Big Bullets inapeza choyamba mmasewero omwe matimuwa anakumana chinali chongowapatsa ndipo chinasokoneza osewera ake.
Iye wayankhula izi atatha masewero omwe agonja 4-0 pa bwalo la Kamuzu kuti atuluke mu chikho cha Castel ndipo wati izi ndi kamba koti chigoli choyamba chinali chabodza.
"Masewero anali abwinobwino ndipo timasewera bwino koma chigoli choyamba cha Bullets anangowapatsa nde chinawakhumudwitsa anyamata anga. Ndi osewera ambiri oti amasewera timu yathu yaing'ono nde nzovuta kusewera ndi Bullets ndikumawapatsa zigoli chonchi." Anatero Chirambo.
Zigoli ziwiri za Hassan Kajoke ndi chimodzi aliyense cha Patrick Mwaungulu ndi Precious Sambani ndi zomwe zathandizira kuti Bullets ipitilire mu ndime Ina. Zateremu, Hammers yamaliza chaka chino ndipo ipita kopumulira.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
"SINDINAGANIZIREKO ZOTI TITULUKA" - CHIRAMBO
Mphunzitsi watimu ya Ekwendeni Hammers, Elias Chirambo, wati ndi wokondwa kamba koti timu yake yatsala mu ligi ya TNM Supa ligi ya chaka chino ndipo wati sanaganizireko zoti atuluka mu ligi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonjetsa Dedza Dynamos 2-1 kuti apulumuke mu ligi ndipo wati anyamata ake analimbikira kwambiri mmasewerowa.
"Anali masewero abwino kwambiri ndipo tithokoze Mulungu kuti tapambana ndipo tili pa mapointsi 36, sindinaganizireko zotuluka mmutu mwangamu kungoti kumpoto tili ndi matimu abwino kwambiri koma kuti thandizo ndi lomwe limasowa kwambiri." Anatero CHIRAMBO.
Timu ya Ekwendeni Hammers inali imodzi mwa matimu omwe anali pa ngozi yotuluka koma chipambanochi chawafikira pa mapointsi 36 pa masewero 30 pa nambala 12.
MPHUNZITSI WAYIMITSIDWA KAMBA KOSOWA KHALIDWE
Timu ya Ekwendeni Hammers yaimitsa wachiwiri kwa mphunzitsi wawo, Luckson Mauluka Nyoni, kamba ka zifukwa zosowa mwambo malingana ndi timuyi.
Timuyi yati mphunzitsiyu anachita zinthu zomwe sizinakomere timuyi pa masewero omwe anagonjetsa Civo United 3-2 pa bwalo la Rumphi sabata yatha ndipo mpake amuyimitsa.
Koma poyankhapo, Nyoni wati sakudziwa za nkhaniyi poti sanalandire kalata iliyonse komanso kuti anatsanzika pamasewero omwe timuyi inagonja 3-1 ndi Silver Strikers basi.
Mauluka ndi mmodzi mwa aphunzitsi omwe akhalitsako kutimuyi kuchokera mu chaka chomwe inalowa mu ligi ndipo timuyi ikumenyera nkhondo yoti isatuluke mu ligiyi.
Source: Wa Mpira
MATIMU AKUMPOTO AKUKANIRANA KUTULUKA
Nkhondo yozimenyera nkhondo yotsala mu ligi ya TNM yavuta kwambiri pomwe timu ya Ekwendeni Hammers yakankhira ku chigwa cha matimu otuluka timu ya Moyale Barracks kutsatira kugonjetsa Civo 3-2 pa bwalo la Rumphi lachitatu.
Sammy Phiri, Wongani Lungu ndi Blessings Singini anagoletsa zigoli za Hammers pomwe Binwell Katinji ndi John Dambuleni anamwetsa za Civo zomwe zinakondweretsa mphunzitsi wa Hammers, Elias Chirambo.
"Tithokoze Mulungu kuti anali mbali yathu komanso tiyamike anyamata kuti asewera bwino mpaka tapambana. Tinali koti titha kutuluka koma tachokako, masewero atsalawa tiyesetsa kuti tidzapambanenso." Anatero Chirambo.
Asanayambe masewerowa, Hammers inali pa nambala 14 koma kutsatira kupambanaku, iwo afika pa nambala 11 ndi mapointsi 33 pa masewero 29 mu ligiyi.
"TIZIBWANA PANG'ONO TATIPWETEKETSA" - MAULUKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Ekwendeni Hammers, Luckson Mauluka Nyoni, wati timu yake inangochita zibwana pang'ono zomwe zachititsa kuti agonje pomwe amasewera ndi Red Lions.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 pa bwalo la Balaka ndipo wati timu yake inali bwino mchigawo choyamba koma Lions inasintha zinthu mu chigawo chachiwiri.
"Anali masewero a zigawo ziwiri, mu chigawo choyamba tinasewera bwino moti tinapeza mipata yochuluka yoti tikanatha kugoletsa koma chigawo chachiwiri Red Lions inabwera, analowetsa winawake kumbaliku yemwe anasinthadi zinthu, ndi tizibwana tinachinyitsa." Anatero Mauluka.
Timu ya Ekwendeni Hammers tsopano ili nawo pa ngozi yoti itha kutuluka mu ligi ya TNM pomwe ili ndi mapointsi 30 pa masewero 27 ndipo ali pa nambala 13 mu ligiyi.
"OSEWERA ANAKOMEDWA NDI SAPOTI YA PANJA" - MAULUKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Ekwendeni Hammers, Luckson Mauluka Nyoni, wati osewera atimu yake anakomedwa ndi ochemerera nthawi yomwe anapeza chigoli chawo zomwe zinachititsa kuti atayilire.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe alepherana 1-1 ndi FCB Nyasa Big Bullets ndipo wati mipata yomwe anaipeza akanagoletsa zikanatha kuwachitira ubwino.
"Anali masewero abwino kwambiri tinapeza mipata yoti tikanagoletsa tikanatha kupambana komabe sizinatheke komabe zotsatira izizi zitilimbikitsa. Atapeza chigoli anakomedwa ndi phokoso la ochemerera nde anatayilira." Anatero Mauluka.
Iye wati timu yake sikungoyang'ana zotsala mu ligi koma kuti ithere mu matimu 8 oyamba mu ligi. Iwo ali pa nambala 13 ndi mapointsi 30 pa masewero 26.
"CHIBWANA NDI CHIMENE CHIKUMATIPWETEKA" - NYONI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Ekwendeni Hammers, Luckson Mauluka Nyoni, wati timu yake yagonja masewero ake ndi MAFCO mu ligi kamba ka chibwana pomwe wati akuphonya mipata kwambiri.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 ndipo wati chibwana cha osewera akafika ku golo la anzawo, akumalangika nacho ku golo kwawo.
"Anali masewero abwino tinapeza mipata yoti tikanatha kupeza zigoli koma tinaphonya nde mukakumana ndi timu yoti ikufuna zigoli imakulanga kumapeto, mwina tizibwana pang'ono koma anyamata asewera bwino." Anatero Nyoni.
Sizikuyendabe ku Ekwendeni pomwe yafika pa nambala 12 ndi mapointsi 29 pa masewero 25 omwe yasewera mu ligiyi.
#Tawonga2023
"SIZINAYAMBE KUOPSA KWENIKWENI" - MAULUKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Ekwendeni Hammers, Luckson Mauluka Nyoni, wati sizinayambe kuopsa kwenikweni ku mbali yawo kuti atha kumadera nkhawa zoti atha kutuluka angakhale kuti zotsatira zikuvuta kutimuyi.
Nyoni amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-1 ndi timu ya Blue Eagles pa bwalo la Nankhaka ndipo wati zigoli zomwe anagoletsetsa zinali zachangu koma amaliza bwino zomwe zikuwapatsa mphamvu.
"Sizinayambe kuopsa kwenikweni, batani la chiopsezo sitinadine nde timenyabe kuti tiyambe kuchita bwino, tasewera bwino makamaka kumapeto nde ndi mmene tathera, titenga zimenezo kuzipititsa mmasewero athu otsatira, ndi achisodzera ndipo akadaphunzira." Anatero Mauluka.
Iye wati akonza molakwika kuti mmasewero awo otsatira adzachite bwino. Hammers ikadali pa nambala 9 pomwe ili ndi mapointsi 28 pa masewero 22 omwe asewera.
"SITIKUYANG'ANA ZOTSALA MU LIGI KOMA TOP 8" - MAULUKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Ekwendeni Hammers, Luckson Mauluka Nyoni, wati chipambano chomwe timuyi yapeza chiwathandiza kubweretsanso mtima wopambana kwa osewera pomwe akuyang'ana zoyambiranso kuchita bwino mu ligi ya TNM.
Mauluka amayankhula izi pomwe timuyi yapambana koyamba mu chigawo chachiwiri pomwe yagonjetsa Extreme FC pa bwalo la Rumphi. Iye wati ndi okondwa kamba ka chipambanochi ndipo zibwenzeretsa mtima wopambana kwa osewera atimuyi.
"Ndife okondwa kamba ka chipambanochi chimene takhala tikuchifuna kwambiri, kupambana kwa lero kutithandiza kuti anyamata abweremo mzimu opambana poti pakatipa anasiya kuzikhulupilira. Sitikuyang'ana zotsala mu ligi komatu kutsala mu top 8." Anatero Mauluka.
Pa masewero 21 yomwe asewera atimuyi, Ekwendeni Hammers yapeza mapointsi okwana 28 ndipo ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8).
HAMMERS IKUFUNA NDALAMA ZAWO
Timu ya Ekwendeni Hammers imayenera kunyamuka lachinayi madzulo kulowera mu mzinda wa Blantyre komwe akuyenera kudzakumana ndi Bangwe All Stars koma alephera pomwe osewera awo anyanyala.
Malipoti aonetsa kuti anyamata atimuyi akufuna ndalama zao zomwe amalandira akapambana masewero zomwe timuyi sinawapatse kwa nthawi tsopano.
Mmodzi mwa anthu akutimuyi, yemwe sanafune kutchulidwa dzina, wati anyamatawa ananetsa kuti sanyamuka ulendowu pokhapokha apatsidwe ndalamazi.
Ekwendeni Hammers ili pa nambala yachisanu mu ligi ya TNM pomwe yatolera ma points 22 pa masewero 13 ndipo idzakumananso ndi Dedza Dynamos lolemba mu chikho cha FDH Bank.
Timu ya Ekwendeni Hammers yati ikufuna kupereka mavuto ku timu ya FCB Nyasa Big Bullets pomwe matimuwa akukumana loweruka mu ligi ya TNM.
Mphunzitsi watimuyi, Luckson Mauluka Nyoni ndiyemwe watero.