Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"OYIMBIRA AMAWATHANDIZAKO A CIVO" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Gilbert Chirwa, wadandaula ndi kayimbilidwe ka Godfrey Nkhakananga ponena kuti amathandizirako timu ya Civo mu ziganizo zake zina.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 ndi Civo pa bwalo la Civo ndipo wati timu yake sinali bwino mchigawo choyamba komabe oyimbira wathandizira Civo.
"Anali masewero ovuta inde tagonja mwina sitinali bwino mchigawo choyamba chifukwa tinabalalika koma mchigawo chachiwiri tinabweramo koma mwina anzathu oyimbirawa anawathandizako a Civo, amapatsa ma free kick komabe tibwereranso tikakonze mavuto athu." Anatero Chirwa.
Timuyi tsopano ili pa nambala yachikhumi ndi chiwiri (12) pomwe ili ndi mapointsi asanu ndi imodzi (6) pa masewero asanu.
"TIKUMAMVETSETSA ANYAMATA POTI NDI ATSOPANO" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Gilbert Chirwa, wati anyamata ake akonzeka kwambiri kuti achite bwino pomwe akukumana ndi timu ya Chitipa United pakhomo pa bwalo la Mulanje Park lamulungu.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa ndipo wati timu yake ikumasewera bwino mmasewero omwe agonjako koma akumawamvetsetsa pakuti ndi atsopano mu ligi ya TNM.
"Masewero omwe takhala tikusewera timachita bwino koma mwina zolakwika zing'onozing'ono ndi zimene zimatipweteketsa koma tikumawakonzabe poti ndi atsopano tikumawamvetsetsa." Anatero Chirwa.
Iye watinso timu ya Chitipa ndi yabwino koma khumbo lawo ndi loti masewero apakhomo azikwanitsa kuchita bwino.
Timu ya FOMO ili pa nambala 12 pomwe yatolera mapointsi atatu pa masewero atatunso omwe yasewera.
"TIKAKHAZIKIKA TIZIPAMBANA MASEWERO" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Gilbert Chirwa, wati timu yake imangopanga zibwana zing'onozing'ono zomwe zachititsa kuti agonje masewero omwe amakumana ndi Kamuzu Barracks.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-1 pa bwalo la Champions ndipo wati tsopano akapeza luntha losewerasewera mu ligiyi ndikukhazikika ayamba kuchita bwino.
"Zoonadi timangochita tizibwana mpake anzathu amachinya zigoli nde ndi zodandaulitsa koma tikuyenera tiphunzire kuti muligi mulibe chisoni nde Poti nkoyamba ambiriwa kusewera ligiyi tikuphunzira ndipo tikakhazikika posachedwapa tiyamba kupeza zipambano tsopano." Anatero Chirwa.
Timu ya FOMO tsopano yagonja kawiri motsatizana ndipo inakwanitsa kupeza chipambano mmasewero oyamba ndipo ili pa nambala yachikhumi ndi mapointsi atatu.
Game yavuta
"WAMKULU AKACHOKA AKULIRA PA MULANJE" - FOMO
Mkulu woona za malonda ku FOMO, Daniel Mbebuwa, wati timuyi ili ndi mapointsi asanu ndi imodzi kale angakhale kuti sanasewere ndi Mighty Mukuru Wanderers ponena kuti Manoma akachoka manja ali mkhosi.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero a matimuwa omwe achitike pa bwalo la Mulanje lamulungu ndipo wachenjeza a Wanderers kuti akonzekere mikango yolusa yokhayokha.
"Ndiwauze kuti sabata yatha tinamasula mikango yaimuna yokha koma apa tikamasula yaimuna ndi yaikazi ndipo akonzeke kudzathamanga, wamkulu adzachoka akulira chifukwa Pano ndi pamanda." Anatero Mbebuwa.
Iye wamema anthu kuti akhamukire ku bwaloli poti kudzakhalanso kugulitsa kwa unifolomu ya timuyi patsikuli.
Timuyi ikuchokera kopambana 1-0 ndi Bangwe All Stars ndipo inakumana ndi Manoma chaka chatha mu Castel Challenge ndipo Wanderers inapambana 1-0.
Noma 2:1fomo prediction
FOMO YAPEZA CHIPAMBANO CHOYAMBA
Timu ya FOMO yapeza chipambano chake choyamba mu ligi ya TNM pomwe yagonjetsa timu ya Bangwe All Stars 1-0 pa bwalo la Mulanje masana a loweruka.
Hassan Luwembe anamwetsa chigoli pa mphindi 77 za masewerowa kuti timuyi ipambane ndipo mphunzitsi wawo Gilbert Chirwa anati ndi okondwa kamba kopambana masewerowa.
"Ndine wokondwa poti tapambana masewerowa ndipo analidi ovuta koma tinawauza anyamatawa kuti alimbikire mpaka anapeza chigoli, Pali ma dera omwe sitinachite bwino koma tikonza mavutowa kuti kupita chitsogolo tipitilire kuchita bwino." Anatero Chirwa.
Timuyi yalowa kumene mu ligiyi ndipo yapanga mbiri popambana masewero awo enieni oyamba mu ligiyi. Timuyi ili pa nambala yachitatu mu ligi ndi mapointsi atatu.
"AKHALA MASEWERO OVUTA KWAMBIRI" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Gilbert Chirwa, wati masewero awo ndi timu ya Bangwe All Stars masana a loweruka akhale ovuta kwambiri koma anyamata ake akonzeka.
Chirwa amayankhula patsogolo pa masewerowa pomwe wati nkofunikira ndikuyamba ndi chipambano kuti akhazikike bwino mu ligi ya TNM.
"Molalo ndi yokwera kwambiri anyamata akonzeka mmasewerowa chilichonse tapanga chatsala ndi choti tikaonetse pa bwalo la zamasewero. Akhala masewero ovuta kwambiri poti Bangwe ndi timu yabwino komabe tikufunika tiyambe ndi kupambana," Anatero Chirwa.
Timu ya FOMO ikhale ikusewera masewero awo oyamba mu ligiyi poti kakhala koyamba kusewera mu ligiyi. Masewerowa Ali pa bwalo la Mulanje lomwe pakhomo pa timuyi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
BWEKE NEARS FOMO MOVE
Former FCB Nyasa Big Bullets forward, Bright Munthali, could return in the TNM Super League in 2024 season as he is about to joining the newly promoted side, FOMO FC.
According to reports, the player has now opened discussions with the Mulanje based side to play for them this season.
Bweke is a free agent after end of contract at AD Vilankulo in Mozambique.
#KasongaJr
NYONI ALI KU FOMO
Wachiwiri kwa mphunzitsi wakale wa Ekwendeni Hammers, Luckson Mauluka Nyoni, tsopano ali ku Mulanje pomwe aphunzitse nawo timu ya FOMO.
Nyoni akhala wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Gilbert Chirwa, mu chaka choyambilira cha mu TNM Supa ligi cha timuyi.
Awiriwa anagwirapo limodzi ntchito ku Ekwendeni Hammers mu 2022 pomwe timuyi inachita bwino koopsa Chirwa asanapite ku Dedza Dynamos.
FOMO YASANKHA BWALO LA MULANJE PARK
Timu imene yangolowa kumene mu Supa ligi, FOMO, yasankha bwalo la Mulanje Park ku bungwe la Football Association of Malawi kuti ndi limene agwiritse ntchito ngati bwalo lawo lapakhomo patsogolo pa ligiyi.
Timuyi yasankha bwaloli poti iyo ndi yaku Mulanje ndipo apereka ku FAM ngati mbali imodzi yokwanilitsa zomwe timu ikuyenera kukhala nazo pa ndondomeko ya Club licensing.
Ndipo woona za ndondomekoyi, a Cassper Jangale, atsimikiza kuti tsopano ayamba kuyendera mabwalo osiyanasiyana mdziko muno kuyambira 26 February ndipo ndandanda wa mabwalo omwe avomerezedwe udzatuluka pa 13 March.
Nayo khonsolo ya mzinda wa Mulanje yati ikukonza zofunikira pa bwaloli kuti likhale pa mulingo wochititsa masewero amu ligi yaikuluyi.
Timuyi imalephera kugwiritsa ntchito bwaloli ikusewera mu ligi yaing'ono kamba ka kusamvana pakati pa iwo ndi khonsoloyi ndipo amakasewera ku bwalo la Esperanza mu mzindawu.
"NDAWAUZA KUTI ATIPEZERE ENA" - CHIRWA
Mphunzitsi yemwe walembedwa kumene kumbali ya timu ya FOMO, Gilbert Chirwa, walonjeza timuyi kuti ichita bwino kwambiri mu chikho cha Supa ligi ndipo wawauza eni ake kuti amupezere osewera atsopano.
Iye amayankhula pomwe amalandilidwa kutimuyi atasaina mgwirizano wa chaka chimodzi nditimuyi yomwe yangolowa kumene kuchokera mu ligi yachigawo chakummwera yomwe anapambana atagonjetsa Ntopwa.
Chirwa, yemwe chaka chatha amaphunzitsa ku Dedza Dynamos, wati wapempha mkulu watimuyi kuti ayesetse kumupezera osewera ena atsopano kuti alimbitse timuyi.
"Pa zokambirana zathu ndinawapempha kuti mwina atipezere osewera ena atsopano kuti alumikizane ndi ena omwe alowetsa timuyi mu Supa ligi, ndikukhulupilira kuti choncho zithandiza kuti timu izichita bwino." Iye anatero.
Iye anatinso kutimu iliyonse yomwe amapita amachita bwino ndipo akuyembekezera kuti ku FOMO zichitanso chimodzimodzi ndipo ikamatha chakachi idzakhala yatsala mu ligiyi. Kumbali ya omuthand
"I WILL ALSO HELP ANOTHER TEAM TO BE PROMOTED" - MSUKWA
FOMO FC head coach, Mapopa Msukwa, has advised the team coach that will cone at the team to beef up the team's squad in few areas in order to perform well in their debut season in the TNM Super League in 2024.
Msukwa said this after guiding the team into the Top flight league thanks to a 4-3 win in penalty shootouts against Ntopwa on Sunday at the Kamuzu Stadium but said he has left the at least in good condition.
"Unfortunately, I will not be with the team in the league because I have CAF C so they will look out for another coach with CAF B or A. The other coach will have to beef up the team but I have left them on a good place, I will maybe go and help another team earn promotion into the Super League again." Said Msukwa.
This will be the first ever time for the Mulanje Based boys to play in the top flight league and they have almost two months to prepare for the 2024 season.
Reported by Hastings Wadza Kasonga Jr
"OYIMBIRA NDI YEMWE WATIPWETEKA" - SOSTEN
Wapampando wa timu ya FOMO FC, Hadweck Sosten, wati timu yake yagonja chifukwa choti oyimbira, Mayamiko Kanjere, amakondera timu ya FCB Nyasa Big Bullets Reserve mmasewerowa.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-1 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati Kanjere akumudziwa kale kuti sayimbira bwino.
"Anali masewero abwino, tamenya bwino kwambiri muone timasunga mpira kwambiri kuposa iwowa timawamenya koma oyimbira ziganizo zake sizinali bwino. Anawapatsa penate yabodza pomwe iwo akagwira samayimba nde iyeyu watipweteka." Anatero Sosten.
Iye watinso timuyi ilowa mu Supa ligi ya chaka cha mawa. Kutsatira kugonjaku, timu ya FOMO ikadali pa nambala yachiwiri mu gulu B ndi mapointsi 33 pa masewero 18.
Fomo win case, to face Nyasa Big Bullets Reserve By Grecium Gama:
Mulanje-based side, Fomo, will face Nyasa Big Bullets Reserve in the semifinal of the Thumbs Up Southern Region Football... times.mw