Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"KUKHALA CHETEKO NDEKUTI TIKUFUFUZA" - BANDA
Mlembi wamkulu wabungwe la Super League of Malawi, Williams Banda, wayankhulapo pa kudandaula kwa timu ya Blue Eagles kuti bungweli silikuyankhabe pa dandaulo lawo chifukwa choti likufufuza.
Banda wayankhula izi kutsatira kudandaula kwa Blue Eagles kuti SULOM ikuchedwa kuwayankha koma iye wati angakhale Blue Eagles yomweyo ikudziwa malamulo okhudza nthawi yomwe bungwe lawo likhonza kuwayankhira.
"Dandaulo likafika ndekuti limapita Ku disciplinary komiti yomwe imayenera kuti ifufuze nde kuchedwako sikuti angokhala koma akufufuza. Zokhudza kuti tiyankha liti pali malamulo omwe angakhale a Blue Eagles akuwadziwa komanso inunso mukuwadziwa." Anatero Banda.
Blue Eagles inalembera SULOM kuti ifufuze zachinyengo pakati pa matimu achisilikali a Red Lions komanso Moyale Barracks omwe anathandizira kuti Blue Eagles ituluke mu ligi ya TNM.
"KODI ZIKUFUNIKA KUTI MAKOCHI TIZIKALOWA M'BWALO?" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wadandaula kuti timu yake inangopereka zigoli pomwe tsopano timuyi yatuluka mu chikho cha Castel atagonja 4-2 ndi Silver Strikers.
Kananji amayankhula atatha masewerowa ndipo wati sakudziwano kuti osewera aziwayankhula motani chifukwa akumachita zosiyana ndi zomwe akuuzidwa ngakhale timu yawo ikumasewera bwino.
"Tivomereze tagonja 4-2 ndi timu ya Silver Strikers, chibwana chimalanda olo mutatenga CR Socials zigoli zomwe tachititsa lero sangachinyitse, tangopereka zigoli nde zikumadabwitsa kuti mwina tizikalowa makochi m'bwalomo chifukwa kuwauza sindikudziwa kuti akuganiza bwanji akumapanga zina." Anatero Kananji.
Zateremu timuyi tsopano yamaliza chaka cha 2023 ndipo ayamba kukonzera umoyo wawo mu ligi yaying'ono ya Chipiku Stores ya chigawo chapakati atatuluka mu ligi ya TNM.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
"TIKUYANG'ANA CASTEL NDIPO AMENEYU TIMWA NDITHU" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya 'Carlsberg Cup' Kananji, wati timu ya Blue Eagles sipita mophweka pomwe akukumana ndi timu ya Silver Strikers mu chikho cha Castel ndipo wati timu yonse ikuyang'ana pa chikho chomwechi.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewerowa pa bwalo la Bingu lachitatu ndipo wati timu ya Silver Strikers isapite moderera kuti iwo anatuluka kamba koti apita ndi mtima onse.
"Ndi masewero ovuta kwambiri ndipo anzathuwo asabwere mophweka kuti mwina poti tinatuluka mu ligi koma kukubwera January anyamata akufunikira ka ndalama koti atuluke nako nde ife maso athu ali pamenepa Castel ameneyu timwa ndithu." Anatero Kananji.
Iye wati anyamata ake anachivomera zoti atuluka mu ligi ndipo onse chidwi chili pa masewero amenewa. Omwe apambane mmasewero amenewa adzakumana ndi Bangwe All Stars mu ndime ya matimu anayi.
BLUE EAGLES IKUFUNA KUSUMIRA MOYALE NDI RED LIONS
Timu ya Blue Eagles kudzera mwa wapampando wawo, Alexander Simenti, ikulingalira zokasumira matimu a Moyale Barracks komanso Red Lions kamba koti ali ndi umboni kuti pa masewero awo panachitika zachinyengo.
Iye amayankhula izi ndi nyuzipepala ya Nation kutsatira kutuluka mu ligi kamba koti Moyale Barracks inatenga mapointsi ambiri pamwamba pa iwo poti anafanana chilichonse pa ndandanda wa matimu.
Blue Eagles inapita mu tsiku lomalizali ili pa nambala 9 koma inagonja 2-1 ndi MAFCO pomwe Moyale Barracks inagonjetsa Red Lions yomwe inali itatuluka kale 7-0 zomwe ambiri akayikira kuti anapatsana poti onse ndi asilikali.
Eagles yauza mkulu woyang'ana za milandu kuti akamang'ale ndi kuti Moyale Barracks ipatsidwe chilango ndi kutulutsidwanso mu ligi.
BLUE EAGLES YATULUKA MU LIGI
Timu ya Blue Eagles yatuluka mu ligi yaikulu ya mdziko muno ya TNM Supa ligi pomwe bungwe la Super League of Malawi latengera yemwe anapeza mapointsi ambiri pa mzake kutsatira kufanana chilichonse ndi timu ya Moyale Barracks.
Blue Eagles inapita mmasewerowa ili pa nambala yachisanu ndi chinayi (9) koma yagonja 2-1 ndi timu ya MAFCO yomwe nayonso inali pa chiopsezo choti itha kutulukanso ndipo Christopher Sibale wati masewero anali ovuta basi.
"Simmene amayenera kukhalira kungoti anali masewero ovuta kwambiri chifukwa anzathuwa nawonso anali pa ngozi komanso kuti anyamata omwe timayembekezera kuti asintha zinthu sanatero nde sizinayende ndi plan yathu." Anatero Sibale asakudziwa kuti atuluka.
Timu ya Moyale yagonjetsa Red Lions 7-0 kuti afanane ma points ndi zigoli ndi Blue Eagles koma Moyale inapambana ndi kufanana mphamvu pa masewero omwe matimuwa anakumana.
Iyo yatsatira Extreme FC komanso Red Lions ku matimu omwe atuluka mu ligi ya chaka cha 2023.
"BLUE EAGLES NDI MAFCO ILI NGATI NDIME YOTSIRIZA" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati akuyembekeza kuti masewero awo ndi timu ya MAFCO lamulungu pa bwalo la Nankhaka akhale ovuta kwambiri poti matimu onse ali ndi zolinga ndi masewerowa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero a matimuwa lamulungu pomaliza ligi ya chaka chino ndipo wati akufunitsitsa kupambana ndi cholinga choti asewere nawo mu ndime ya matimu asanu ndi atatu a Airtel Top 8 a chaka cha mawa.
"Kukonzekera kwathu kwayenda bwino ndipo tachilimika chifukwa tikukakumana ndi MAFCO yomwe timavutitsana nayo nde masewero ake akhala ngati a ndime yotsiriza komabe kusewera kwake ndi komwe taonetsa kumapetoku, kungoika mtima kuti chaka cha mawa tidzasewere mu Airtel Top 8." Anatero Kananji.
Timuyi ili pa nambala 10 mu ligiyi ndi mapointsi 35 pa masewero 29 ndipo kupambana ndi MAFCO kutha kudzawatengera pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7).
"KB IMATITENGA NGATI AZIKAZAWO NDE TINATOPA" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati timu yake inakonzeka bwino kwambiri patsogolo pa masewero awo ndi Kamuzu Barracks ndipo anayeneradi kuti apambane.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa KB 3-1 pa bwalo la Civo lachinayi ndipo wati timuyi inatopa kugonja ndi timuyi ndipo apa inabwera ndi mtima wonse kuti ipambane.
"Tithokoze Mulungu komanso tithokoze anyamata athu kamba koti tachita bwino, KB imatitenga ngati azikazi awo tikakumana amangotimenya koma apa tinangoti mmene tinamenyera ndi Bullets tikapite chomwecho nde tinakonzekadi ndipo anyamata achita kunenadi kuti tawathamangitsa." Anatero Kananji.
Blue Eagles yakhala timu yachisanu ndi chiwiri (7) kuti ifike mu ndime ya matimu asanu ndi atatu a Castel Challenge Cup ndipo idzakumana ndi timu ya Silver Strikers mu ndimeyi.
"TIKAKUMANA AMAKHALA MASEWERO OSANGALATSA" - SIBALE
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Christopher Sibale, wati akuyembekeza masewero apamwamba kwambiri ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets pomwe wati matimuwa akakumana amakhala masewero osangalatsa.
Iye amayankhula patsogolo pa kukumana kwa matimuwa pa bwalo la Bingu mu ndine ya matimu anayi amu chikho cha Airtel Top 8 ndipo wati akonzekera bwino masewerowa.
"Akhala masewero osangalatsa komanso ovuta kwambiri chifukwa tikakumana ndi anzathuwa amakhala masewero ovuta kwambiri komabe ndi masewero aku chikho ndi wofunika kukalimbikira kuti tikafike mu ndime yotsiriza." Anatero Sibale.
Matimuwa anakumananso mu ndime yotsiriza ya chikhochi mu chaka cha 2018 pomwe Blue Eagles inapambana 1-0 kuti atenge chikhochi ndipo mangawa amenewo akadalipobe kumbali ya Bullets.
"BWENZI TIKUTI BLUE EAGLES YAPEZA 3 POINTS" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati timu yake inasewera mwapamwamba moti ikanatha kupambana mmasewero omwe yalepherana ndi FCB Nyasa Big Bullets koma mipata yomwe anayipeza aphonya.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe alepherana 0-0 pa bwalo la Nankhaka ndipo wati zolakwika zonse akonza kuti mmasewero awo ndi MAFCO adzapambane.
"Tiyamike Mulungu kuti takumana ndi anzathu a Nyasa Big Bullets, tithokozenso anyamata athu asewera bwino kwambiri mwina zangochitika koma bwenzi tikuti Blue Eagles yatenga 3 points koma tikonza molakwika kuti ndi MAFCO tidzapambane." Anatero Kananji.
Kutsatira zotsatirazi, Blue Eagles yasuntha mu ligi ya TNM pomwe tsopano yafika pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) ndi mapointsi 35 pa masewero 29 mu ligiyi.
"TIKANGOMENYA EXTREME BASI TIDZAKUMANA 2024" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati masewero omwe timu yake ikukumana ndi Extreme FC loweruka akhala ovuta kwambiri koma chipambano ndi chofunikira kwambiri.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe ali pa bwalo la Nankhaka ndipo wati akapambana masewero amenewa, akhala kuti apulumuka basi.
"Ndi masewero ovuta kwambiri poti anzathuwa zatsimikizika kuti tsopano atuluka mu ligi nde alibe phuma lililonse zomwe zivutitse masewerowa komabe tawauza anyamata kuti kupambana titseka zoyankhula zonse tikapanda kutero atiyikadi mmagulu aja omati tili pa chiopsezo chotuluka koma kungopambana basi tidzakumana mu 2024." Anatero Kananji.
Blue Eagles ili pa nambala 10 mu ligi ya TNM pomwe ili ndi mapointsi 31 pa masewero 26 omwe yasewera mu ligiyi.
"TINANGOYIWERENGA MU ZOFOOKA ZAWO" - SIBALE
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Christopher Sibale, wati kutenga point imodzi pamwamba pa Chitipa United ndi yofunikira kamba koti iwasuntha ndi mmene ligi yavutiramu.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe afanana mphamvu 2-2 pa bwalo la Karonga lolemba ndipo wati iwo anagwiritsa ntchito kuiona malo omwe akufooka kuti apeze zigoli zawo.
"Tinaona momwe akufooka nchifukwa chake tinapeza chigoli mwa changu kwambiri ndipo kumapeto tinawaona kuti atopa nde tinatenga ena ammbali kuti apite pakati kuti tichulukepo mpake tinapeza chigoli chobwenzera chija." Anatero Sibale.
Kutsatira kupeza point imeneyi, Eagles yasuntha kufika pa nambala 11 ndi mapointsi 31 pa masewero 26 omwe yasewera.
#KasongaJr
ZILANGO KU SULOM ZAYAMBA POMWE EAGLES YALANDIRA
Bungwe loyendetsa ligi yaikulu mdziko muno ya Super League of Malawi lapereka chilango kwa osewera anayi a timu ya Blue Eagles komanso wothandizira mphunzitsi watimuyi, Christopher Sibale, kamba koyambitsa zisokonezo pomwe ankasewera ndi Ekwendeni Hammers ku Mzuzu.
Mu kalata imene bungweli latulutsa lolemba lapereka chilango kwa kwa osewera atimuyi monga Sankhani Mkandawire, Tonic Viyuyi, Chakonda Majanga komanso Ranken Mwale kuti apereke K500,000 kamba kofuna kumenya oyimbira ndipo Mwale amupatsa chilango chosasewera masewero anayi.
Sibale naye alipira ndalama yokwana K500,000 kamba kochita nkhalidwe loyipa ndipo Blue Eagles ilipira ndalama zokwana K1.5 million kamba kokanika kuteteza anthu awo.
Ndalamayo ikuyenera kuperekedwa pasanathe masiku 14 ndipo pa mlanduwu, Blue Eagles inathamangitsa oyimbira kamba kosakhutira ndi kayimbilidwe mmasewero omwe anagonja 1-0 ndi Ekwendeni Hammers.
"NGAKHALE DEDZA YACHITA KUTI TINAKUMANA NAZO" - KANANJI.
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati timu yake inasewera bwino kwambiri koma zavuta ndi kukanika kugoletsa ndi chifukwa chake agonja masewero awo 2-1 ndi Dedza Dynamos.
Iye amayankhula izi atatha masewerowa ndipo wati timu yake ndi imene inasewera bwino kuposa Dedza Dynamos koma chibwana cha osewera chawapweteketsa.
"Anali masewero abwino kwambiri anyamata analimbikira koma tizibwana pang'ono ta anyamatawa ndi timene tatipweteketsa, anzathuwa anangobwera ndi kutichinya koma tinawapanikiza ndithu ndipo akuchita kunena okha kuti lero anakumana nazo." Anatero Kananji.
Iye wati kutaya mapointsi kukupereka ntchito yaikulu koma mavuto awo awakonza. Blue Eagles ikadali pa nambala 10 ndi mapointsi 30 pa masewero 25 omwe yasewera.
"TIGWIRITSA NTCHITO MWAYI WOSEWERA PAKHOMO" - SIBALE
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Christopher Sibale, wati masewero awo ndi Mighty Mukuru Wanderers lachitatu likudzali pa bwalo la Nankhaka akhala ovuta koma iwo agwiritsa ntchito mwayi wosewera pakhomo.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewerowa ndipo wati masewerowa akhala ovuta ndipo atapambana masewero anayi otsogozana, iye wati osewera asazitenge kuti afikapo.
"Ndi masewero ovuta kwambiri koma zitengera kuti ifeyo takonzeka motani ndipo tikufunikira chipambano kuti tipitilire kukwerabe kumtunda kuja nde anyamata akonzeka kwambiri. Ifeyo takonzeka koma kwambiri tigwiritsa ntchito mwayi wa pakhomo, tili pakhomo nde tikufunikira chipambano." Anatero Sibale.
Blue Eagles ikapambana masewerowa ifika pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe padakali pano ali ndi mapointsi 30 pa masewero 23 omwe yasewera mu ligiyi.
#Tawonga2023
"AWA AKHALA MAYESERO KUTI TIDZIWE POMWE TITHERE" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati masewero atimuyi pakati pa Red Lions lero komanso ndi Mighty Mukuru Wanderers lachitatu likudzali ali ngati mayesero kwa iwo kuti awaone mbali imene athere mu ligi ya chaka chino.
Kananji amayankhula izi patsogolo pa masewero awo ndi Red Lions pa bwalo la Balaka ndipo wati akuyembekeza kuti masewero awo akhala ovuta kwambiri. Iye wati akapambana masewero awo awiriwa atsimikizadi kuti satuluka mu ligi.
"Akhala masewero ovuta kamba koti tonse tikuvutika komanso titakumana pa Nankhaka tinalepherana 1-1 komabe anyamata tawauza kufunikira kopeza chipambano mmasewero awa ndi a Wanderers chifukwa ali ngati mayesero kuti tione mbali yomwe tithere. Tikapambana onse, zotuluka mu ligi sizitikhudza nawo." Kananji anafotokoza.
Timu ya Blue Eagles ili pa nambala 10 mu ligi ya chaka chino pomwe yatolera mapointsi 27 pa masewero 22 ndipo ngati ipambane lero, ifika pa nambala 10.
"SIKUTI ZAYERA KOMA TICHILIMIKABE" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati timu yake sinapezebe mtendere ndipo akuyenera kuchilimika angakhale atalikirana ndi nambala za matimu otuluka mu ligi.
Kananji amayankhula izi atatha masewero omwe apambana 2-1 ndi timu ya Ekwendeni Hammers pa bwalo la Nankhaka ndipo wati anawapempha osewera ake kuti apambane chifukwa Ekwendeni imawavuta kwambiri.
Iye wati anyamata ake akumvera zimene akuuzidwa koma wati asatayilire chifukwa mtendere sunawachokere.
"Yakhala ili nyimbo kuti tikuyenera kuchoka kumunsi tili kuja nde padakali pano ligi yavuta nde anyamata sakuyenera kugona komabe tikuyesetsa kuti tichokeretu." Anatero Kananji.
Timu ya Blue Eagles yafika pa nambala 10 mu ligiyi pomwe tsopano ili ndi mapointsi 27 pa masewero 22 amu ligiyi.
"NDINANENA KALE KUTI BLUE EAGLES SINGATULUKE" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, watsindika kuti timu yawo singatuluke mu ligi ya TNM ndipo anthu ayionanso ikusewera momwemu chaka cha mawa.
Kananji amayankhula izi atatha masewero omwe apambana 1-0 ndi Civo ku bwalo la Champions ndipo wati masewero anali ovuta koma chigoli cha msanga chawathandiza. Iye wati anyamata ake tsopano akubweramo pa mmene amafunira.
"Chichitikireni mkumano wathu uja, tapambani iyiyi yachiwiri ndipo tafanana mphamvu imodzi zomwe zikusonyeza kuti anyamata akubweramo ndipo tichita bwino. Ndinanena kale kuti nzosatheka kuti timu yathu ikhonza kutuluka mu ligi." Anafotokoza Kananji.
Timu ya Blue Eagles ili pa nambala yachikhumi ndi chiwiri (12) pomwe yatolera mapointsi okwana 24 pa masewero 21 omwe asewera.
KUSINTHA KUKUONEKA KU EAGLES
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Christopher Sibale, wati timu yake yayamba kuonetsa kusintha pomwe ayamba kutolera mapointsi mmasewero omwe asewera posachedwa.
Eagles inagonjetsa Mighty Wakawaka Tigers ndipo yafanana mphamvu mmasewero awo sabata yatha ndipo patsogolo pa masewero awo ndi Civo United pa bwalo la Champions ku Dowa, Sibale wati akonzeka.
"Tinafika mu Lilongwe ndipo tayamba kukonzekera masewero ndi Civo, zikuoneka kuti zinthu zayamba kuyenda ndipo zitati zipitilire ndekuti tikhonza kuchoka kumunsi kumene tili kuja." Anatero Sibale.
Timu ya Blue Eagles ikadali ku chigwa cha matimu otuluka mu ligi pomwe ili pa nambala 14 ndi mapointsi 21 pa masewero 20.
"OYIMBIRA AKUMATENGA MBALI PA MASEWERO" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati oyimbira mmasewero awo ndi Karonga United anatenga gawo lina lolepheretsa kuti apambane koma kutenga point imodzi koyenda ndi chamuna.
Kananji amayankhula izi atatha masewerowa omwe matimuwa analepherana 0-0 pa bwalo la Karonga ndipo wayamikira osewera ake kamba kozipereka mmasewerowa.
"Tithokoze Mulungu kuti tasewera ndi Karonga United, tiwayamikirenso anyamata athu agwira ntchito yotamandika, tinabwera ndipo tinayesetsa kuti mwina tipeze chipambano komabe achina Newton akumatenga mbalinso yaikulu bola asamakhale ndi mbali." Kananji anafotokoza.
Iye wati point yomwe atenga mmasewerowa iwathandize kupita patsogolo ndipo wati pang'onopang'ono akhale akuyendabe kuthawa chigwa cha matimu otuluka. Eagles yafika pa nambala 13 ndi mapointsi 21 mmasewero 20.
"TIKUYENERA KUPAMBANA MASEWEROWA" - SIBALE
Mphunzitsi wachiwiri kutimu ya Blue Eagles, Christopher Sibale, wati timu yake ikuyenera kupambana masewero awo ndi timu ya Karonga United ndi cholinga choti achoke kumunsi kwa ligi komwe iwo ali.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewero omwe aliko pa bwalo la Karonga lamulungu ndipo wati akudziwa kuti akhale ovuta chifukwa choti Karonga ikuchita bwino.
"Akhala masewero ovuta poti Karonga ikuchita bwino komabe ife takhonzeka kuti tikachite bwino, anyamata tawauza kuti akapita kutsogolo azigwiritsa ntchito mwayi uliwonse omwe aziupeza." Anatero Sibale.
Iye wati chipambano mtsiku la lero chikhale chabwino kwambiri poti timuyi ichoka kumunsi komwe iwo ali ndikuti asadzatuluke mu ligi ya TNM.
Eagles ili pa nambala yachitatu kuchokera kumunsi pomwe ali ndi mapointsi 20 pa masewero 19 omwe asewera mu ligi ya chaka chino.