Timu ya Nyasa Big Bullets masanawa ikumana ndi Sable Farming pa bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre.
Mphunzitsi wa Bullets, Kalisto Pasuwa, wati timu yake ndi yakonzeka kuchita bwino pa masewero.
A Pasuwa ali ndi chikhulupiliro kuti osewera ake alimbikira kuti atenge mapoint onse atatu.
Padakali pano, Bullets ili pa nambala 1 ndi mapoint 38 pa masewero 14 omwe yasewera pamene Sable Farming ili ndi mapoint 11 pa masewero 13 omwe yasewera ndipo ili pa number 14.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores