Mtsogoleri wa bungwe loyendesa masewero a mpira wamiyendo mdziko muno la FAM Walter Nyamilandu walangiza adindo oyendesa masewero-wa kupewa kugwilitsa ntchito mphamvu zawo molakwika.
A Nyamilandu anena izi potsegulira mkumano wa adindo oyendesa masewero a mpira wamiyendo omwe ukuchitikira ku Mangochi.
Iwo ati ngati mtsogoleri umayenera kulunjika pokonza zinthu, kupanga ubale wabwino ndi ogwira ntchito onse komanso kuwatsogolera ku zinthu zabwino.
Pamkumano-wu omwe uchitike kwa masiku awiri, adindowa aphunzira momwe angagwilire ntchito yawo mwaukadaulo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores