Timu ya Nyasa Big Bullets imagwilitsa ntchito ndalama zokwana K15 million kuti lizigwilitsa ntchito bwalo la Blantyre Sports Club pa chaka.
Mmodzi wa akuluakulu ku Bullets, Fleetwood Haiya, wanena izi pamene ali ndi malingaliro omanga bwalo komanso ofesi mu mzinda wa Blantyre.
A Haiya ati lingaliro lithandizira kuchepesa ndalama zomwe amagwilitsa ntchito pa chaka kuphatikiza K15 million yomwe amalipira malo a ofesi zawo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores