Timu ya Karonga United yati mphunzitsi wakale wa timuyi Oscar Kaunda akuyenera kubwenza ndalama zokwana K620, 000 zomwe analandira ku timuyi pa nthawi yomwe amagwira ntchito yake.
Mlembi wa Karonga United Ramsy Simwaka wati izi ndi zomwe akuluakuku agwilizana pa mkumano omwe unalipo masiku apitawa.
Iwo ati apereka chikalata chololeza mphunzitsi kuyamba kugwira ntchito ku timu ina pokhapokha akabwenza ndalamazi.
A Kaunda ati anatenga K450, 000 yomwe anagwilitsa ntchito kuchoka ku Blantyre, K50, 000 analipilira nyumba ndipo K120, 000 anagulira phone.
Padakali pano Oscar Kaunda akuphunzitsa ku timu ya Civil Service United.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores